2 Kings 23:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Farao Neko wa ku Ejipito adaika Eliyakimu, mwana wa Yosiya, kuti akhale mfumu m'malo mwa bambo wake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Farao Neko adatenga Yehowahazi kupita naye ku Ejipito, ndipo adafera komweko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wake, nasanduliza dzina lake likhale Yehoyakimu; koma anapita naye Yehowahazi, nafika iye m'Ejipito, nafa komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao Neko anayika Eliyakimu mwana wa Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwa abambo ake Yosiya, ndipo anasintha dzina lake kukhala Yehoyakimu. Koma iye anatenga Yehowahazi kupita naye ku Igupto ndipo anakafera kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao-Neko analonga ufumu Eliyakimu mwana wa Yosiya, m'malo mwa Yosiya atate wace, nasanduliza dzina lace likhale Yoyakimu; koma anapita naye Yoahazi, nafika iye m'Aigupto, nafa komweko.