2 Kings 23:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoyakimu nayenso ankapereka siliva ndi golide kwa Farao. Komatu ankachita kukhometsa msonkho m'dziko mwakemo kuti apereke ndalamazo kwa Farao, monga momwe Farao adamlamulira. Ankatenga siliva amene anthu am'dzikomo ankayenera kukhoma, pamodzi ndi golide yemwe, malinga ndi chuma cha munthu aliyense, ndipo ankazipereka kwa Farao Neko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehoyakimu anapereka siliva ndi golide kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golide, yense monga mwa kuyesedwa kwake, kuzipereka kwa Farao Neko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyakimu anapereka kwa Farao Neko siliva ndi golide amene anamufuna uja. Koma kuti iye apereke zimenezi, amankhometsa msonkho mʼdziko mwakemo ndipo amalandira siliva ndi golide kuchokera kwa anthu a mʼdzikomo molingana ndi chuma cha munthu aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoyakimu anapereka siliva ndi golidi kwa Farao, koma anasonkhetsa dzikoli lipereke ndalamazi; monga mwa lamulo la Farao anasonkhetsa anthu a m'dziko siliva ndi golidi, yense monga mwa kuyesedwa kwace, kuzipereka kwa Farao-Neko.