2 Kings 23:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Zebida, mwana wa Pedaya, wa ku Ruma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Zebuda, mwana wa Pedaya wa ku Ruma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoyakimu anali wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Zebida mwana wa Pedaya wa Ruma.