2 Kings 23:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adachotsa fano la Asera m'Nyumba ya Chauta, napita nalo kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni. Tsono adalitenthera ku mtsinje wa Kidroniko, naliperapera, nkutaya phulusa lake pa manda a anthu wamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natulutsa chifanizocho m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nachitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nachipera chikhale fumbi, naliwaza fumbi lake pa manda a ana a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturutsa cifanizoco m'nyumba ya Yehova kunja kwa Yerusalemu ku mtsinje wa Kidroni; nacitenthera ku mtsinje wa Kidroni, nacipera cikhale pfumbi, naliwaza pfumbi lace pa manda a ana a anthu.