2 Kings 23:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosiya adabwera nawo ansembe a ku mizinda ya ku Yuda, naononga akachisi opembedzerako mafano kumene ansembe aja ankaperekera nsembe, kuyambira ku Geba mpaka ku Beereseba. Adagwetsa akachisi onse amene anali pa chipata cha khomo la Yoswa, nduna ya mzindawo. Maloŵa anali ku dzanja lamanzere la khomo la mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natulutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa chipata cha Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa chipata cha mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naturutsa ansembe onse m'midzi ya Yuda, nawaipitsira misanje, imene ansembe adafukizapo zonunkhira, kuyambira Geba kufikira Beereseba; napasula misanje ya kuzipata, yokhala polowera pa cipata ca Yoswa kazembe wa mudzi, yokhala ku dzanja lako lamanzere kwa cipata ca mudzi.