2 Kings 23:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe a ku akachisiwo sadaŵalole kufika ku guwa la Chauta ku Yerusalemu, komabe ankadya nao buledi wosatupitsa ndi ansembe anzao kumeneko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ansembe a misanje sanakwere kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda chotupitsa pakati pa abale ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ansembe a misanje sanakwera kudza ku guwa la nsembe la Yehova ku Yerusalemu; koma anadya mkate wopanda cotupitsa pakati pa abale ao.