2 Kings 24:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi ya Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo Yehoyakimu adakakamizidwa kutumikira Nebukadinezarayo zaka zitatu. Koma pambuyo pake Yehoyakimuyo adapandukira Nebukadinezara.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku ake Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni anakwerako, Yehoyakimu nagwira mwendo wake zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku ace Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwerako, Yoyakimu nagwira mwendo wace zaka zitatu; pamenepo anatembenuka nampandukira.