2 Kings 24:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehoyakini mfumu ya ku Yuda adadzipereka kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi mai wake, alangizi ake, nduna zake ndiponso akuluakulu a kunyumba kwake. Mfumu ya ku Babiloni idamgwira Yehoyakini ukapolo pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehoyakini mfumu ya Yuda anatulukira kwa mfumu ya Babiloni, iye ndi make, ndi anyamata ake, ndi akalonga ake, ndi adindo ake; mfumu ya Babiloni nimtenga chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyakini mfumu ya Yuda pamodzi ndi amayi ake, atumiki ake, anthu ake olemekezeka ndiponso akuluakulu onse anadzipereka kwa mfumu ya ku Babuloni. Mfumu ya Babuloni inagwira Yoyakini ukapolo mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Yoyakini mfumu ya Yuda anaturukira kwa mfumu ya Babulo, iye ndi mace, ndi anyamata ace, ndi akalonga ace, ndi adindo ace; mfumu ya Babulo nimtenga caka cacisanu ndi citatu ca ufumu wace.