2 Kings 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatenga anthu onse a ku Yerusalemu, ndiye kuti nduna zonse ndi anthu onse amphamvu. Onsewo pamodzi analipo 10,000. Adatenganso anthu onse aluso ndi amisiri osula. Sadatsalepo ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu osauka okha am'dzikomo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacoka nao a m'Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsala ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okha okha a m'dziko.