2 Kings 24:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayenso Yehoyakini adamtenga kupita naye ku Babiloni. Adatenganso mai wake wa mfumuyo, akazi ake, nduna zake ndiponso anthu omveka am'dzikomo. Onsewo adaŵagwira ukapolo ku Yerusalemu kunka nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebukadinezara anatenga Yehoyakini ngati kapolo kupita naye ku Babuloni. Mu Yerusalemu anatenganso amayi a mfumu, akazi ake, akuluakulu ake ndiponso anthu olemekezeka mʼdzikomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacoka naye Yoyakini kumka naye ku Babulo, ndi mace wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ace, ndi omveka a m'dziko; anacoka nao andende ku Yerusalemu kumka nao ku Babulo.