2 Kings 24:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumu ya ku Babiloni idalonga ufumu Mataniya, malume wa Yehoyakini, m'malo mwake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu ya Babiloni analonga Mataniya mbale wa atate wake akhale mfumu m'malo mwake, nasanduliza dzina lake likhale Zedekiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye analonga ufumu Mataniya, malume wa Yoyakini mʼmalo mwake ndipo anasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu ya Babulo analonga Mataniya mbale wa atate wace akhale mfumu m'malo mwace, nasanduliza dzina lace likhale Zedekiya.