2 Kings 24:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya, wa ku Libina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zedekiya anali wa zaka makumi awiri mphambu cimodzi polowa ufumu wace, nakhala mfumu zaka khumi ndi cimodzi m'Yerusalemu; ndi dzina la mace ndiye Hamutala mwana wa Yeremiya wa ku Libina.