2 Kings 24:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adatumiza magulu ankhondo a Ababiloni, a Asiriya, a Amowabu, ndi a Aamoni kuti akathire nkhondo Yuda, mpaka kuwononga dzikolo, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa atumiki ake aneneri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Ababiloni, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amowabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova adawanena ndi dzanja la atumiki ake aneneriwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anamtumizira magulu a Akasidi, ndi magulu a Aaramu, ndi magulu a Amoabu, ndi magulu a ana a Amoni, nawatumiza pa Yuda kuliononga, monga mwa mau a Yehova: adawanena ndi dzanja la atumiki ace aneneriwo.