2 Kings 24:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidachitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pake; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake. Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwa mkwiyo wa Yehova zonse zidacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda, mpaka adawataya pamaso pace; ndipo Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.