2 Kings 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi, zimenezi zidagwera Yuda, monga momwe Chauta adaalamulira. Adachotsa Ayudawo pamaso pake, chifukwa cha zoipa zimene mfumu Manase ankachita,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zedi ichi chinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwachotsa pamaso pake, chifukwa cha zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazichita;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu, izi zinachitikira Yuda monga momwe Yehova analamulira nʼcholinga choti awachotse pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase ndi zonse zimene anachita,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zedi ici cinadzera Yuda mwa lamulo la Yehova, kuwacotsa pamaso pace, cifukwa ca zolakwa za Manase, monga mwa zonse anazicita;