2 Kings 24:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Ejipito sidatulukenso m'dziko lake, poti mfumu ya ku Babiloni inali italanda maiko onse a mfumu ya ku Ejipito kuchokera ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje wa Yufurate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mfumu ya Aejipito sinabwerezanso kutuluka m'dziko lake, pakuti mfumu ya Babiloni idalanda kuyambira ku mtsinje wa Ejipito kufikira ku mtsinje Yufurate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mfumu ya Aigupto sinabwerezanso kuturuka m'dziko lace, pakuti mfumu ya Babulo idalanda kuyambira ku mtsinje wa Aigupto kufikira ku mtsinje Firate, ndilo lonse anali nalo mfumu ya Aigupto.