2 Kings 24:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Nehusita, mwana wa Elinati, wa ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la make ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yoyakini anali wa zaka khumi mphambu zisanu ndi zitatu polowa iye ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu; ndi dzina la mace ndiye Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu.