2 Kings 25:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni. Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse, kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wake, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, iye ndi khamu lake lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babulo, iye ndi khamu lace lonse anadzera Yerusalemu, naumangira misasa, naumangira timalinga mouzinga.