2 Kings 25:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaathaŵa kupita kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi ena otsala, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi anthu otsalira m'mudzi, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babiloni, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkulu wa olindirira anamuka nao andende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi anthu otsalira m'mudzi, ndi opanduka akuthawira kwa mfumu ya Babulo, ndi aunyinji otsalira, Nebuzaradani mkuru wa olindirira anamuka nao andende.