2 Kings 25:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵawo, napita nawo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ake, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Ababiloni anazithyolathyola, natenga mkuwa wake kunka nao ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zoimiritsa zamkuwa zinali m'nyumba ya Yehova, ndi maphaka ace, ndi thawale lamkuwa, zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazithyolathyola, natenga mkuwa wace kumka nao ku Babulo.