2 Kings 25:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Msinkhu wa nsanamira imodzi unali mamita asanu ndi atatu, ndipo pamwamba pake panali mutu wamkuŵa. Msinkhu wa mutuwo unali mita imodzi ndi theka. Ukonde wake pamodzi ndi makangaza ake, zonsezo zinali zamkuŵa, ndipo zinali pamwamba pa mutu uja mozungulira. Nsanamira yachiŵiri inali yolingana ndi inayo, ndipo inalinso ndi ukonde.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Msinkhu wake wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pake mutu wamkuwa; ndi msinkhu wake wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzake inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Msinkhu wace wa nsanamira imodzi ndiwo mikono khumi mphambu isanu ndi itatu, ndi pamwamba pace mutu wamkuwa; ndi msinkhu wace wa mutuwo ndiwo mikono itatu, ndi ukonde, ndi makangaza pamutu pouzinga, zonse zamkuwa; ndi nsanamira inzace inali nazo zomwezo pamodzi ndi ukonde.