2 Kings 25:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso anthu asanu amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankapemba anthu am'dzikomo ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
natenga m'mudzimo mdindo woikidwa woyang'anira ankhondo; ndi anthu asanu a iwo openya nkhope ya mfumu opezeka m'mudzimo; ndi mlembi, kazembe wa nkhondo wolembera anthu a m'dziko; ndi anthu a m'dziko makumi asanu ndi limodzi opezeka m'mudzimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika