2 Kings 25:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumuyo idalamula kuti aŵakwapule ndi kuŵaphera ku Ribula, m'dziko la Hamati. Umu ndimo m'mene Ayuda adatengedwera ukapolo kuŵachotsa ku dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Niwakantha mfumu ya Babiloni, niwaphera ku Ribula m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwachotsa m'dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha. Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Niwakantha mfumu ya Babulo, niwaphera ku Ribila m'dziko la Hamati. Motero anamuka nao Ayuda andende kuwacotsa m'dziko lao.