2 Kings 25:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atsogoleri Achiyuda ndi ankhondo ao onse amene anali atathaŵa, atamva kuti mfumu ya ku Babiloni idaika Gedaliya kuti akhale kazembe, adadza kwa Gedaliya ku Mizipa, iwo pamodzi ndi anthu ao. Atsogoleriwo maina ao anali aŵa: Ismaele mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yazaniya mwana wa Maakati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babulo adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismayeli mwana wa Netaniya, ndi Yohanana mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmakati, iwo ndi anthu ao omwe.