2 Kings 25:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 37 cha kutengedwa ukapolo Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27 la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babiloni, pa chaka choyamba cha ufumu wake, adakomera mtima Yehoyakiniyo nammasula m'ndende.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri cha kumtenga ndende Yehoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya Babiloni anamuweramutsa mutu wake wa Yehoyakini mfumu ya Yuda atuluke m'kaidi, chaka cholowa iye ufumu wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali caka ca makumi atatu mphambu zisanu ndi ziwiri ca kumtenga ndende Yoyakini mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi ziwiri, tsiku la makumi awiri mphambu asanu ndi awiri la mwezi, Evili Merodaki mfumu ya Babulo anamuweramutsa mutu wace wa Yoyakini mfumu ya Yuda aturuke m'kaidi, caka colowa iye ufumu wace;