2 Kings 25:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo mfumu Zedekiya adathaŵa usiku pamodzi ndi ankhondo ake onse kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzinda wonsewo. Ndipo adaloŵera cha ku Araba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku chipata cha pakati pa makoma awiri, ili ku munda wa mfumu; Ababiloni tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kuchidikha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo linga la mudziwo linagamulidwa, nathawira ankhondo onse usiku, njira ya ku cipata ca pakati pa makoma awiri, iri ku munda wa mfumu; Akasidi tsono anali pamudzi pouzinga; nimuka mfumu pa njira ya kucidikha.