2 Kings 25:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma gulu lankhondo la ku Babiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nkhondo ya Ababiloni inalondola mfumu, niipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yake yonse inambalalikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nkhondo ya Akastdi inalondola mfumu, niipeza m'zidikha za Yeriko; koma nkhondo yace yonse inambalalikira.