2 Kings 25:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya, ndipo adamkolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo, nkupita naye ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napha ana a Zedekiya pamaso pace, namkolowola Zedekiya maso ace, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka nave ku Babulo.