2 Kings 25:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi mwa alangizi ake, adadza ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwezi wachisanu, tsiku lachisanu ndi chiwiri la mweziwo, ndicho chaka chakhumi mphambu chisanu ndi chinai cha mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, Nebuzaradani mkulu wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babiloni, anadza ku Yerusalemu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwezi wacisanu, tsiku lacisanu ndi ciwiri la mweziwo, ndico caka cakhumi mphambu cisanu ndi cinai ca mfumu Nebukadinezara mfumu ya Babulo, Nebuzaradani mkuru wa olindirira, ndiye mnyamata wa mfumu ya Babulo, anadza ku Yerusalemu,