2 Kings 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka cha 18 cha ufumu wa Yehosafati m'dziko la Yuda, Yoramu mwana wa Ahabu, adaloŵa ufumu wa ku Israele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka khumi ndi ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele m'Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israyeli m'Samariya m'caka cakhumi mphambu zisanu ndi zitatu ca Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.