2 Kings 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu Yehosafati adafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri woti angatithandize kupempha nzeru kwa Chauta?” Mmodzi mwa atsogoleri a gulu la ankhondo la mfumu Yoramu adayankha kuti, “Aliko Elisa, mwana wa Safati, amene anali mtumiki wa Eliya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israele anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?” Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehosafati anati, Palibe pano mneneri wa Yehova kodi, kuti tifunsire Yehova mwa iye? Ndipo wina wa anyamata a mfumu ya Israyeli anayankha, nati, Elisa mwana wa Safati ali pano, ndiye uja anathira madzi m'manja a Eliya.