2 Kings 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Elisa adafunsa mfumu Yoramu kuti “Inu kwanga kuno mwadzatani? Bwanji osapita kwa aneneri amene bambo wanu ndi mai wanu ankapemphako nzeru.” Koma Yoramu adati, “Iyai, pakuti Chauta ndiye amene waitana mafumu atatufe, kuti atipereke m'manja mwa Amowabu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anati kwa mfumu ya Israele, Ndili ndi chiyani ndi inu? Mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israele inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Mowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.” Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anati kwamfumuya Israyeli, Ndiri ndi ciani ndi inu? mukani kwa aneneri a atate wanu, ndi kwa aneneri a amai wanu. Koma mfumu ya Israyeli inanena naye, Iai, pakuti Yehova anaitana mafumu ife atatu kutipereka m'dzanja la Moabu.