2 Kings 3:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adati, “Pali Chauta Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamtumikira, pakadapanda kuti ndimamchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikadakusamalani ngakhale kukuyang'anani komwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pake, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anati, Pali Yehova wa makamu, amene ndiima pamaso pace, ndikadapanda kusamalira nkhope ya Yehosafati mfumu ya Yuda, sindikadakuyang'anitsani, kapena kukuonani.