2 Kings 3:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoramu ankachimwira Chauta, koma kuipa kwake sikudafanefane ndi kwa bambo wake ndi kwa mai wake Yezebele. Yoramuyo adagumula fano la Baala limene bambo wake adaamanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita choipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wake ndi amake; pakuti anachotsa choimiritsa cha Baala adachipanga atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita coipa pamaso pa Yehova, koma osati monga atate wace ndi amace; pakuti anacotsa coimiritsa ca Baala adacipanga atate wace.