2 Kings 3:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Amowabu atamva kuti mafumu atatu abwera kuti achite nawo nkhondo, adaitana onse amene ankatha kumenya nkhondo kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu. Onsewo adakandanda ku malire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atamva tsono Amowabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'chuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atamva tsono Amoabu onse kuti adakwera mafumu aja kuthirana nao nkhondo, anamemeza onse akumanga lamba m'cuuno ndi okulapo, naima iwo m'malire.