2 Kings 3:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amowabuwo atadzuka m'mamaŵa pamene dzuŵa linkaŵala pa madzi, adaona madzi ali psuu ngati magazi kutsogolo kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amowabu madzi ali pandunji pao ali psu ngati mwazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anauka mamawa dzuwa linawala pamadzipo, naona Amoabu madzi ali pandunji pao ali psyu ngati mwazi;