2 Kings 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Amowabu aja atafika ku zithando za Aisraele, Aisraelewo adaŵathira nkhondo, iwowo nkuyamba kuthaŵa. Koma Aisraele aja ankapha Amowabuwo akuŵapirikitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israele, Aisraele ananyamuka, nakantha Amowabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anafika ku misasa ya Israyeli, Aisrayeli ananyamuka, nakantha Amoabu, nathawa iwo pamaso pao; ndipo analowa m'dziko ndi kukantha Amoabu.