2 Kings 3:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele adagumula mizinda yao, ndipo pa munda uliwonse wachonde aliyense ankaponyapo mwala, mpaka minda yonse idadzaza ndi miyala. Adatseka akasupe onse, nagwetsa mitengo yonse yabwino. Kudatsala mzinda wa Kiri-Haresefi wokha, koma pambuyo pake ankhondo oponya miyala adabwera naugonjetsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napasula midzi, naponya yense mwala wake panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yake m'Kiri-Haresefi mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napasula midzi, naponya yense mwala wace panthaka ponse pabwino, naidzaza, nafotsera zitsime zonse zamadzi, nagwetsa mitengo yonse yabwino, kufikira anasiya miyala yace m'Kirihasereti mokha; koma oponya miyala anauzinga, naukantha.