2 Kings 3:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho idatenga mwana wake wachisamba amene adaayenera kudzaloŵa ufumu wake, nimpereka pa linga ngati nsembe yopsereza kwa mulungu wa Amowabu. Zimenezi zidadzetsa ukali waukulu wokwiyira Aisraele, mwakuti iwo adangoithaŵa mfumuyo, nabwerera ku dziko lakwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anagwira mwana wake wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwake, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israele kwambiri; potero anamchokera, nabwerera ku dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anagwira mwana wace wamwamuna woyamba amene akadakhala mfumu m'malo mwace, nampereka nsembe yopsereza palinga. Ndipo anakwiyira Israyeli kwambiri; potero anamcokera, nabwerera ku dziko lao.