2 Kings 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kale Mesa, mfumu ya Amowabu, ankaŵeta nkhosa. Ndipo chaka ndi chaka ankapereka ngati msonkho kwa mfumu ya Israele anaankhosa okwanira 100,000, ndiponso ubweya wa nkhosa zamphongo 100,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mesa mfumu ya Mowabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israele ubweya wa anaankhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mesa mfumu ya Moabu anali mwini nkhosa, akapereka kwa mfumu ya Israyeli ubweya wa ana a nkhosa zikwi zana limodzi, ndi wa mphongo zikwi zana limodzi.