2 Kings 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Yoramuyo adatumiza mau kwa Yehosafati, mfumu ya ku Yuda, kuti, “Mfumu ya Amowabu yandigalukira ine. Kodi sungapite nane kunkhondo, kuti tikamenyane ndi Amowabu?” Tsono Yehosafatiyo adayankha kuti, “Ndidzapita. Ine ndi iwe ndife amodzi, anthu anga ndi ako omwe, akavalo anga ndi akonso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Mowabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Mowabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?” Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nakatumiza mau kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mfumu ya Moabu wapandukana ndi ine; kodi udzamuka nane kukathira nkhondo pa Moabu? Nati, Ndidzakwera: ine ndikhala ngati iwe, anthu anga ngati anthu ako, akavalo anga ngati akavalo ako.