2 Kings 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mfumu ya ku Israele pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda kudzanso mfumu ya ku Edomu, onsewo adapita limodzi. Ndipo atayenda mozungululira m'chipululu masiku asanu ndi aŵiri, kunalibe madzi oti amwe asilikali pamodzi ndi nyama zosenza katundu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka mfumu ya Israele, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka mfu mu ya Israyeli, ndi mfumu ya Yuda, ndi mfumu ya Edomu, nazungulira njira ya masiku asanu ndi awiri; ndipo panalibe madzi kuti ankhondo amwe, kapena nyama zakuwatsata.