2 Kings 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adauza mtumiki wake Gehazi kuti aitane maiyo. Gehazi adamuitana maiyo, ndipo adafika kwa Elisa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa mtumiki wake Gehazi, “Muyitane Msunemuyu.” Ndipo anapita kukamuyitana mayiyo, ndipo anabwera nayima pamaso pa Elisa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa Gehazi mnyamata wace, Itana Msunemu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pace.