2 Kings 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adalamula Gehazi kuti amuuze maiyo kuti, “Ndithu mwavutika potichitira zonsezi. Nanga ife tikuchitireni chiyani? Kodi muli ndi mau oti tikakunenereni kwa mfumu, kapena kwa mtsogoleri wankhondo?” Maiyo adayankha kuti, “Ine ndimakhala mwaufulu pakati pa anthu a mtundu wanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’ ” Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikucitire iwe ciani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.