2 Kings 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Elisa adauza mai uja kuti, “Pa nthaŵi yonga yomwe ino chaka chamaŵachi, mudzakhala mukululuza mwana wamwamuna.” Ndipo maiyo adati, “Pepani mbuyanga, inu munthu wa Mulungu, musandinamizetu ine mdzakazi wanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Nyengo yino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anati kwa mayiyo, “Nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, udzakhala utanyamula mwana wamwamuna mʼmanja mwako.” Mayiyo anatsutsa zimenezi nanena kuti, “Ayi mbuye wanga. Inu munthu wa Mulungu, musanamize mdzakazi wanu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Nyengo yino caka cikudzaci udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, lai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.