2 Kings 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mai uja adaimadi ndipo chaka chotsatira, nthaŵi ngati yomweyo, adabala mwana wamwamuna, monga momwe Elisa adaamuuzira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mayi uja anakhala woyembekezera, ndipo chaka chotsatiracho, nthawi ngati yomweyo anabereka mwana wamwamuna monga momwe Elisa anamuwuzira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo caka cimene cija Elisa adanena naye.