2 Kings 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Elisa adafunsa maiyo kuti, “Nanga mukuti ineyo nditani? Tanenani, muli ndi chiyani m'nyumba mwanu?” Maiyo adayankha kuti, “Mdzakazi wanune ndilibe nkanthu komwe m'nyumba, koma kambiya ka mafuta basi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m'nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?” Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikucitire ciani? undiuze m'nyumba mwako muli ciani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m'nyumba, koma mtsuko wa mafuta.