2 Kings 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adamunyamula, nakampereka kwa mai wake. Mwanayo adakhala pamiyendo pa mai wake mpaka masana, basi nkumwalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namnyamula, napita naye kwa amake. Ndipo anakhala pa maondo ake kufikira usana, namwalira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namnyamula, napita naye kwa amace. Ndipo anakhala pa maondo ace kufikira usana, namwalira.