2 Kings 4:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mkazi uja adanyamula mwana wake nakwera ku chipinda cham'mwamba chija, nakamgoneka pa bedi la Elisa, mtumiki wa Mulungu uja, nkumtsekera momwemo, iye nkutuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, natuluka, namtsekera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, naturuka, namtsekera.