2 Kings 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaitanitsa mwamuna wake, namuuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu wa Mulungu uja, nkubwerakonso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Naitana mwamuna wace, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi buru mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.